[1] Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:
[2] Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo; kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
[3] kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru, akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
[4] Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera, achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
[5] Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake, ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
[6] kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo, mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.
[7] Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
[8] Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
[9] Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
[10] Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa usamawamvere.
[11] Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa;
[12] tiwameze amoyo ngati manda, ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje.
[13] Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;
[14] Bwera, chita nafe maere, ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”
[15] Mwana wanga, usayende nawo pamodzi, usatsagane nawo mʼnjira zawozo.
[16] Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha, amathamangira kukhetsa magazi.
[17] Nʼkopanda phindu kutchera msampha mbalame zikuona!
[18] Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe; amangodzitchera okha msampha!
[19] Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza; chumacho chimapha mwiniwake.
[20] Nzeru ikufuwula mu msewu, ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;
[21] ikufuwula pa mphambano ya misewu, ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,
[22] “Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti? Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti? Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
[23] Tamverani mawu anga a chidzudzulo. Ine ndikukuwuzani maganizo anga ndi kukudziwitsani mawu anga.
[24] Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera. Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.
[25] Uphungu wanga munawunyoza. Kudzudzula kwanga simunakusamale.
[26] Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto; ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
[27] Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe, tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu, mavuto ndi masautso akadzakugwerani.
[28] “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha; mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.
[29] Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova,
[30] popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa.
[31] Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.
[32] Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo, ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.
[33] Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata; adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”