[1] Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu, koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.
[2] Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova, koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.
[3] Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa, koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.
[4] Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
[5] Maganizo a anthu olungama ndi owongoka, koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.
[6] Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa, koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.
[7] Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika, koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.
[8] Munthu amatamandidwa malinga ndi nzeru zake, koma anthu amitima yokhota amanyozedwa.
[9] Nʼkwabwino kukhala munthu wonyozeka koma wodzigwirira ntchito nʼkukhala ndi zonse zofunika, kuposa kukhala wodzikuza koma ulibe ndi chakudya chomwe.
[10] Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake, koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.
[11] Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.
[12] Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa, koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.
[13] Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa; koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.
[14] Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.
[15] Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino, koma munthu wanzeru amamvera malangizo.
[16] Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo, koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.
[17] Woyankhula zoona amapereka umboni woona, koma mboni yabodza imafotokoza zonama.
[18] Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga, koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.
[19] Mawu woona amakhala mpaka muyaya koma mawu abodza sakhalitsa.
[20] Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo; koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.
[21] Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama, koma munthu woyipa mavuto samuthera.
[22] Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
[23] Munthu wochenjera amabisa nzeru zake, koma munthu wopusa amaonetsa uchitsiru wake poyera.
[24] Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira, koma aulesi adzakhala ngati kapolo.
[25] Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu, koma mawu abwino amamusangalatsa.
[26] Munthu wolungama amatsogolera mnansi wake, koma ntchito za anthu oyipa zimawasocheretsa.
[27] Munthu waulesi sapeza chimene akufuna, koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengo wapatali.
[28] Mʼnjira yachilungamo muli moyo; koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.