Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:43

[1] Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.

[2] Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

[3] Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala; koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.

[4] Wochita zinthu mwaulesi amasauka, koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.

[5] Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru, koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.

[6] Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama, koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.

[7] Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso, koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.

[8] Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.

[9] Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka; koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.

[10] Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto, koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.

[11] Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo, koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.

[12] Udani umawutsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

[13] Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu, koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.

[14] Anzeru amasunga chidziwitso koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.

[15] Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.

[16] Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama, koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.

[17] Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo, koma wonyoza chidzudzulo amasochera.

[18] Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.

[19] Mawu akachuluka zolakwa sizisowa, koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.

[20] Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.

[21] Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri; koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.

[22] Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

[23] Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa, koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.

[24] Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira; chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.

[25] Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa, koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.

[26] Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso, ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.

[27] Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo; koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.

[28] Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe, koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.

[29] Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino, koma wochita zoyipa adzawonongeka.

[30] Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.

[31] Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru, koma lilime lokhota lidzadulidwa.

[32] Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula, koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.

Miyambo — Chapters