Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:55

[1] Usamanyadire za mawa, pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.

[2] Munthu wina akutamande, koma osati wekha; mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.

[3] Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri, koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.

[4] Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa. Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.

[5] Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino kuposa chikondi chobisika.

[6] Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino, koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.

[7] Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi, koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.

[8] Munthu amene wasochera ku nyumba kwake, ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.

[9] Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.

[10] Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako, ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto; mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.

[11] Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga; pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.

[12] Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.

[13] Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.

[14] Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri, anthu adzamuyesa kuti akutemberera.

[15] Mkazi wolongolola ali ngati mvula yamvumbi.

[16] Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.

[17] Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake, chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.

[18] Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake, ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.

[19] Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi, chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.

[20] Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta.

[21] Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo, chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.

[22] Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo ndi musi ngati chimanga, uchitsiru wakewo sudzachoka.

[23] Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili. Kodi usamalire bwino ziweto zako?

[24] Paja chuma sichikhala mpaka muyaya, ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.

[25] Pamene udzu watha, msipu nʼkumera; ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,

[26] ana ankhosa adzakupatsani chovala ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.

[27] Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri kuti muzidya inuyo ndi banja lanu ndi kudyetsa antchito anu aakazi.

Miyambo — Chapters