Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:51

[1] Ngati ukhala pansi kuti udye pamodzi ndi wolamulira, uyangʼane bwino zimene zili pamaso pako,

[2] ngati ndiwe munthu wadyera udziletse kuti usaonetse dyera lakolo.

[3] Usasirire zakudya zake, pakuti zimenezo ndi zakudya zachinyengo.

[4] Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma, ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.

[5] Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo. Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

[6] Usadye chakudya cha munthu waumbombo, usalakalake zakudya zake zokoma;

[7] paja iye ndi munthu amene nthawi zonse amaganizira za mtengo wake ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,” koma sakondweretsedwa nawe.

[8] Udzasanza zimene wadyazo ndipo mawu ako woyamikira adzapita pachabe.

[9] Usayankhule munthu wopusa akumva, pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.

[10] Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye,

[11] paja Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu; iye adzawateteza pa milandu yawo kutsutsana nawe.

[12] Mtima wako uzikhala pa malangizo ndipo makutu ako azimvetsera mawu a chidziwitso.

[13] Usaleke kumulangiza mwana; ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.

[14] Ukamukwapula ndi tsatsa udzapulumutsa moyo wake.

[15] Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru, inenso mtima wanga udzakondwera.

[16] Mtima wanga udzakondwera pamene ndidzakumva ukuyankhula zolungama.

[17] Mtima wako usachite nsanje ndi anthu ochimwa, koma uziopa Yehova tsiku ndi tsiku.

[18] Ndithu za mʼtsogolo zilipo ndipo chiyembekezo chakocho sichidzalephereka.

[19] Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.

[20] Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.

[21] Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi ndipo aulesi adzavala sanza.

[22] Mvera abambo ako amene anakubala, usanyoze amayi ako pamene akalamba.

[23] Gula choonadi ndipo usachigulitse; ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.

[24] Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu; Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.

[25] Abambo ndi amayi ako asangalale; amene anakubereka akondwere!

[26] Mwana wanga, undikhulupirire ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.

[27] Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama; ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza.

[28] Amabisala ngati mbala yachifwamba, ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.

[29] Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo? Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?

[30] Ndi amene amakhalitsa pa mowa, amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.

[31] Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akuwira mʼchikho pamene akumweka bwino!

[32] Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amajompha ngati mphiri.

[33] Maso ako adzaona zinthu zachilendo ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.

[34] Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.

[35] Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe! Andimenya koma sindinamve kanthu! Kodi ndidzuka nthawi yanji? Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”

Miyambo — Chapters