[1] Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake:
[2] Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga? Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro?
[3] Usapereke mphamvu yako kwa akazi. Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu.
[4] Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu, mafumu sayenera kumwa vinyo. Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa
[5] kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko, nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka.
[6] Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa, vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;
[7] amwe kuti ayiwale umphawi wawo asakumbukirenso kuvutika kwawo.
[8] Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.
[9] Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.
[10] Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.
[11] Mtima wa mwamuna wake umamukhulupirira ndipo mwamunayo sasowa phindu.
[12] Masiku onse a moyo wake mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino zokhazokha osati zoyipa.
[13] Iye amafunafuna ubweya ndi thonje; amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.
[14] Iye ali ngati sitima zapamadzi za anthu amalonda, amakatenga chakudya chake kutali.
[15] Iye amadzuka kusanache kwenikweni; ndi kuyamba kukonzera a pa banja pake chakudya ndi kuwagawira ntchito atsikana ake antchito.
[16] Iye amalingalira za munda ndi kuwugula; ndi ndalama zimene wazipeza amalima munda wamphesa.
[17] Iye amavala zilimbe nagwira ntchito mwamphamvu ndi manja ake.
[18] Iye amaona kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse.
[19] Iye amadzilukira thonje ndipo yekha amagwira chowombera nsalu.
[20] Iye amachitira chifundo anthu osauka ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.
[21] Iye saopa kuti banja lake lifa ndi kuzizira pa nyengo yachisanu; pakuti onse amakhala atavala zovala zofunda.
[22] Iye amadzipangira yekha zoyala pa bedi pake; amavala zovala zabafuta ndi zapepo.
[23] Mwamuna wake ndi wodziwika pa chipata cha mzinda, ndipo amakhala pakati pa akuluakulu a mʼdzikomo.
[24] Iye amasoka nsalu zabafuta nazigulitsa; amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.
[25] Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake; ndipo amaseka osaopa zamʼtsogolo.
[26] Iye amayankhula mwanzeru, amaphunzitsa anthu mwachikondi.
[27] Iye amayangʼanira makhalidwe a anthu a pa banja lake ndipo sachita ulesi ndi pangʼono pomwe.
[28] Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala; ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,
[29] “Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana koma iwe umawaposa onsewa.”
[30] Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa; koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.
[31] Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.