Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:20

[1] Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole, ngati walonjeza kumulipirira mlendo,

[2] ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena, wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako.

[3] Tsono popeza iwe mwana wanga wadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse: pita msanga ukamupemphe mnansi wako; kuti akumasule!

[4] Usagone tulo, usawodzere.

[5] Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje, ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka.

[6] Pita kwa nyerere, mlesi iwe; kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu!

[7] Zilibe mfumu, zilibe woyangʼanira kapena wolamulira,

[8] komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola.

[9] Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe? Kodi tulo tako tidzatha liti?

[10] Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono ndingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule,

[11] umphawi udzakugwira ngati mbala ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba.

[12] Munthu wachabechabe, munthu woyipa, amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa,

[13] amatsinzinira maso ake, namakwakwaza mapazi ake ndi kulozaloza ndi zala zake,

[14] amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo ndipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu.

[15] Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa; adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa.

[16] Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:

[17] maso onyada, pakamwa pabodza, manja akupha munthu wosalakwa,

[18] mtima wokonzekera kuchita zoyipa, mapazi othamangira msanga ku zoyipa,

[19] mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.

[20] Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.

[21] Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse, uzimangirire mʼkhosi mwako.

[22] Ukamayenda, zidzakulozera njira; ukugona, zidzakulondera; ukudzuka, zidzakuyankhula.

[23] Paja malamulo awa ali ngati nyale, malangizowa ali ngati kuwunika, ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo moyo weniweni,

[24] kukupulumutsa kwa mkazi wadama, zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere.

[25] Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake, asakukope ndi zikope zake,

[26] paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse.

[27] Kodi munthu angathe kutenga moto zovala zake osapsa?

[28] Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto mapazi ake osapserera?

[29] Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina. Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa.

[30] Paja anthu sayinyoza mbala ikaba chifukwa chakuti ili ndi njala.

[31] Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri, ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake.

[32] Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru. Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.

[33] Adzalandira mabala ndi mʼnyozo, ndipo manyazi ake sadzamuchokera.

[34] Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa, ndipo sadzachita chifundo pobwezera.

[35] Iye savomera dipo lililonse; sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani.

Miyambo — Chapters