Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:14

[1] Kodi nzeru sikuyitana? Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?

[2] Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira, imayima pa mphambano ya misewu.

[3] Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda, pa makomo olowera imafuwula kuti,

[4] Inu anthu, ndikuyitana inu; ndikuyitanatu anthu onse.

[5] Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera; inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.

[6] Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri; ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.

[7] Pakamwa panga pamayankhula zoona ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.

[8] Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama; mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.

[9] Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona; kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.

[10] Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva, nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.

[11] Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.

[12] Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera. Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.

[13] Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.

[14] Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino; ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.

[15] Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira. Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.

[16] Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula. Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.

[17] Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza.

[18] Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.

[19] Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.

[20] Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.

[21] Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.

[22] “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba. Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.

[23] Ndinapangidwa kalekalelo, pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.

[24] Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi, zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.

[25] Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo, mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,

[26] lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake; lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.

[27] Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga, pamene ankalemba malire a nyanja yozama,

[28] pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,

[29] pamene anayikira nyanja malire kuti madzi asadutse malirewo, ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.

[30] Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku, kusangalala nthawi zonse pamaso pake.

[31] Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”

[32] “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni; odala anthu amene amasunga njira zanga.

[33] Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru; musanyozere mawu anga.

[34] Wodala munthu amene amandimvera, amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku, kudikirira pa chitseko changa.

[35] Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo ndipo Yehova amamukomera mtima.

[36] Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha; onse amene amandida amakonda imfa.”

Miyambo — Chapters