[1] Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake, koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.
[2] Munthu amapeza zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake, koma anthu osakhulupirika amalakalaka zachiwawa basi.
[3] Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake, koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.
[4] Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, koma munthu wakhama adzalemera.
[5] Munthu wolungama amadana ndi zabodza, koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi.
[6] Chilungamo chimateteza munthu wangwiro, koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.
[7] Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse; munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri.
[8] Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake, koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.
[9] Nyale ya munthu wolungama ndi yokondweretsa, koma nyale ya munthu woyipa imazimitsidwa.
[10] Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano, koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru.
[11] Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.
[12] Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.
[13] Amene amanyoza malangizo adzawonongeka, koma amene amasamala lamulo amalandira mphotho.
[14] Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo; amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.
[15] Munthu wa nzeru zabwino amapeza kuyanja pakati pa anthu, koma munthu wosakhulupirika adzawonongeka.
[16] Munthu wochenjera amachita zinthu mwanzeru, koma chitsiru chimaonetsa poyera uchitsiru wake.
[17] Wamthenga woyipa amagwetsa anthu mʼmavuto, koma nthumwi yodalirika imabweretsa mtendere.
[18] Wokana mwambo adzasauka ndi kunyozedwa, koma wosamala chidzudzulo adzalemekezedwa.
[19] Chinthu chochilakalaka chikachitika chimasangalatsa mtima, koma zitsiru zimadana ndi kuleka zoyipa.
[20] Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru; koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.
[21] Choyipa chitsata mwini, koma wochita zolungama adzalandira mphotho yabwino.
[22] Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa, koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.
[23] Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amachilanda.
[24] Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda, koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.
[25] Munthu wolungama amakhala ndi zakudya zoti adye nʼkukhuta, koma mʼmimba mwa munthu woyipa mumakhala pululu ndi njala.