[1] Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.
[2] Amene amayenda molungama amaopa Yehova, koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova.
[3] Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana, koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza.
[4] Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya, koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso.
[5] Mboni yokhulupirika sinama, koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.
[6] Wonyoza anzake amafunafuna nzeru koma osayipeza, koma munthu womvetsa bwino amadziwa zinthu msanga.
[7] Khala kutali ndi munthu wopusa chifukwa sudzapeza mawu a nzeru.
[8] Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake. Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe.
[9] Zitsiru zimanyoza za kulapa machimo, awo, koma kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.
[10] Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake, ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake.
[11] Nyumba ya munthu woyipa idzapasuka, koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.
[12] Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa.
[13] Ngakhale poseka mtima utha kumva kuwawa, ndipo mathero achimwemwe akhoza kukhala chisoni.
[14] Munthu wosakhulupirika adzalandira zogwirizana ndi ntchito yake, koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito yake.
[15] Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake.
[16] Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa, koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala.
[17] Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru, ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo.
[18] Anthu opusa amalandira uchitsiru, koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu.
[19] Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino, ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama.
[20] Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda, koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri.
[21] Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.
[22] Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika.
[23] Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu, koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.
[24] Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe, koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru.
[25] Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo, koma mboni yabodza imaphetsa.
[26] Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.
[27] Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo, kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.
[28] Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu, koma popanda anthu kalonga amawonongeka.
[29] Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake.
[30] Mtima wodekha umapatsa thupi moyo, koma nsanje imawoletsa mafupa.
[31] Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.
[32] Anthu oyipa adzakanthidwa chifukwa cha ntchito zawo zomwe, koma olungama adzatetezedwa mwa imfa yawo.
[33] Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu, koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru.
[34] Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
[35] Mfumu imasangalatsidwa ndi wantchito wanzeru, koma imachitira ukali wantchito wochititsa manyazi.