Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:56

[1] Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri; kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide.

[2] Wolemera ndi wosauka ndi ofanana; onsewa anawalenga ndi Yehova.

[3] Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.

[4] Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.

[5] Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha, koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.

[6] Mwana muzimuphunzitsa njira yake, ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

[7] Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.

[8] Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto, ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka.

[9] Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.

[10] Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha; mapokoso ndi zonyoza zidzaleka.

[11] Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino, adzakhala bwenzi la mfumu.

[12] Maso a Yehova amakhala pa anthu odziwa bwino zinthu, koma Iye adzalepheretsa mawu a anthu osakhulupirika.

[13] Munthu waulesi amati, “Kunjaku kuli mkango. Ine ndidzaphedwa mʼmisewu!”

[14] Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama; amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.

[15] Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana, koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.

[16] Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake, ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.

[17] Utchere khutu lako ndipo umvere mawu anzeru; uyike mtima wako pa zimene ndikukuphunzitsa kuti udziwe.

[18] Zidzakhala zokondweretsa ngati uzisunga mu mtima mwako ndi wokonzeka kuziyankhula.

[19] Ndakuphunzitsa zimenezi lero koma makamaka uziopa Yehova.

[20] Kodi suja ndinakulembera malangizo makumi atatu okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,

[21] malangizo okudziwitsa zolungama ndi zoona ndi kuti ukawayankhe zoona amene akutumawo?

[22] Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu,

[23] pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo.

[24] Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya

[25] kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake ndi kukodwa mu msampha.

[26] Usakhale munthu wopereka chikole kapena kukhala mboni pa ngongole;

[27] ngati ulephera kupeza njira yolipirira adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.

[28] Usasunthe mwala wamʼmalire akalekale amene anayikidwa ndi makolo ako.

[29] Kodi ukumuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzatumikira mafumu; sadzatumikira anthu wamba.

Miyambo — Chapters