Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:00

[1] Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri, adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.

[2] Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa, koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.

[3] Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake, koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.

[4] Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo, koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.

[5] Munthu woshashalika mnzake, akudziyalira ukonde mapazi ake.

[6] Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake, koma wochita chilungamo amayimba lokoma.

[7] Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi.

[8] Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda, koma anthu anzeru amaletsa ukali.

[9] Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru, chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.

[10] Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro koma anthu olungama amasamalira moyo wake.

[11] Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.

[12] Ngati wolamulira amvera zabodza, akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.

[13] Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti: Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.

[14] Ngati mfumu iweruza osauka moyenera, mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.

[15] Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.

[16] Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka, koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.

[17] Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.

[18] Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo; koma wodala ndi amene amasunga malamulo.

[19] Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi; ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.

[20] Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.

[21] Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana, potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.

[22] Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano, ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.

[23] Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

[24] Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe; amalumbira koma osawulula kanthu.

[25] Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha, koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.

[26] Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima, koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.

[27] Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo; koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.

Miyambo — Chapters