[1] Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere, kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano.
[2] Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi, ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale.
[3] Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo, koma Yehova amayesa mitima.
[4] Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa; munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza.
[5] Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake; amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa.
[6] Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
[7] Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru, nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu?
[8] Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo; kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera.
[9] Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi; wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi.
[10] Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.
[11] Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi; ndipo bwana adzamutumizira wamthenga wankhanza.
[12] Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana ake kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.
[13] Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino, ndiye choyipa sichidzachoka mʼnyumba mwake.
[14] Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi, choncho uzichokapo mkangano usanayambe.
[15] Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa, zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa.
[16] Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsiru poti iyeyo mutu wake sumayenda bwino?
[17] Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse, ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.
[18] Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole ndipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake.
[19] Wokonda zolakwa amakonda mkangano, ndipo wokonda kuyankhula zonyada amadziyitanira chiwonongeko.
[20] Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino; ndipo woyankhula zachinyengo amagwa mʼmavuto.
[21] Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake, abambo a chitsiru sakhala ndi chimwemwe.
[22] Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino, koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.
[23] Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri kuti apotoze chiweruzo cholungama.
[24] Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru, koma chitsiru chimwazamwaza maso ake pa dziko lonse lapansi.
[25] Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake ndipo amapweteketsa mtima amayi ake.
[26] Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa, kapena kulanga anthu osalakwa.
[27] Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu, ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu.
[28] Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete; ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.