[1] Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.
[2] Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
[3] Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.
[4] Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
[5] Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo, koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.
[6] Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa, koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.
[7] Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso. Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.
[8] Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto, koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.
[9] Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake, koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.
[10] Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera, ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.
[11] Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima, koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.
[12] Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru, koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.
[13] Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi; koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.
[14] Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.
[15] Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere.
[16] Mkazi wodekha amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.
[17] Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.
[18] Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu, koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.
[19] Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo, koma wothamangira zoyipa adzafa.
[20] Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.
[21] Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa, koma anthu olungama adzapulumuka.
[22] Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba, ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa.
[23] Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha, koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu.
[24] Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe; wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe.
[25] Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera; iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.
[26] Anthu amatemberera womana anzake chakudya, koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho.
[27] Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo, koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.
[28] Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota, koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.
[29] Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto, ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.
[30] Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo, ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.
[31] Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi, kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!