Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:10

[1] Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova; Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.

[2] Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo, koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.

[3] Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.

[4] Maso odzikuza ndi mtima wonyada, zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.

[5] Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake; koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.

[6] Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.

[7] Chiwawa cha anthu oyipa chidzawawononga, pakuti iwo amakana kuchita zolungama.

[8] Njira ya munthu wolakwa ndi yokhotakhota, koma makhalidwe a munthu wosalakwa ndi olungama.

[9] Nʼkwabwino kukhala wekha pa ngodya ya denga la nyumba, kuposa kukhala mʼnyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.

[10] Munthu woyipa amalakalaka zoyipa; sachitira chifundo mnansi wake wovutika.

[11] Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru; koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.

[12] Zolingalira za munthu woyipa nʼzosabisika pamaso pa Yehova, ndipo Iye adzawononga woyipayo.

[13] Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.

[14] Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo, ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa.

[15] Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala, koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.

[16] Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.

[17] Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

[18] Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima.

[19] Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.

[20] Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma wopusa amachiwononga.

[21] Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika, amapeza moyo ndi ulemerero.

[22] Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.

[23] Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake sapeza mavuto.

[24] Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,” iye amachita zinthu modzitama kwambiri.

[25] Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito.

[26] Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri, koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.

[27] Nsembe ya anthu oyipa imamunyansa Yehova, nanji akayipereka ndi cholinga choyipa!

[28] Mboni yonama idzawonongeka, koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.

[29] Munthu woyipa amafuna kudzionetsa ngati wolimba mtima, koma munthu wowongoka amaganizira njira zake.

[30] Palibe nzeru, palibe kumvetsa bwino, palibenso uphungu, zimene zingapambane Yehova.

[31] Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Yehova amene amapambanitsa.

Miyambo — Chapters