Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:13

[1] Ndipo Yobu anayankha kuti,

[2] “Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona. Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?

[3] Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye, Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe.

[4] Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka. Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka?

[5] Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa, ndipo amawagubuduza ali wokwiya.

[6] Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake ndipo amanjenjemeretsa mizati yake.

[7] Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala; Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi.

[8] Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba ndipo amayenda pa mafunde a pa nyanja.

[9] Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana, nsangwe ndi kumpotosimpita.

[10] Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingawerengeke.

[11] Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona; akadutsa, sindingathe kumuzindikira.

[12] Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa? Ndani anganene kwa Iye kuti, ‘Mukuchita chiyani?’

[13] Mulungu sabweza mkwiyo wake; ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake.

[14] “Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji? Ndingawapeze kuti mawu oti nʼkutsutsana naye?

[15] Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe; ndikanangopempha chifundo kwa woweruza wanga.

[16] Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera, sindikhulupirira kuti akanamva mawu angawo.

[17] Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho, ndipo akanandipweteka popanda chifukwa.

[18] Mulungu sakanandilola kuti ndipumenso koma akanandichulukitsira zowawa.

[19] Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi! Ndipo tikanena za chiweruzo cholungama, ndani angamuzenge mlandu?

[20] Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa; ndikanakhala wopanda cholakwa, pakamwa panga pakanandipeza wolakwa.

[21] “Ngakhale ine ndili wosalakwa, sindidziyenereza ndekha; moyo wanga ndimawupeputsa.

[22] Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Iye amawononga anthu osalakwa ndi anthu oyipa omwe.’

[23] Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi, Iye amaseka tsoka la munthu wosalakwayo.

[24] Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipa Iye amawatseka maso anthu oweruza dzikolo. Ngati si Iyeyo, nanga ndani?

[25] “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro; masikuwo amapita ine osaonapo zabwino.

[26] Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja, ngati mphungu zothamangira nyama zoti zidye.

[27] Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga, ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’

[28] ndikuopabe mavuto anga onse, popeza ndikudziwa kuti simudzavomereza kuti ndine wosalakwa.

[29] Popeza ndapezeka kale wolakwa ndivutikirenji popanda phindu?

[30] Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambiri ndi kusamba mʼmanja mwanga ndi sopo,

[31] mutha kundiponyabe pa dzala, kotero kuti ngakhale zovala zanga zomwe zidzandinyansa.

[32] “Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha, sindingathe kutsutsana naye mʼbwalo la milandu.

[33] Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu, kuti atibweretse ife tonse pamodzi,

[34] munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa ine kuti kuopsa kwake kusandichititsenso mantha!

[35] Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo, koma monga zililimu, sindingathe.

Yobu — Chapters