[1] Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
[2] “Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu? Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?
[3] Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama? Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?
[4] “Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula, kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
[5] Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu? Kodi machimo ako si opanda malire?
[6] Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa; umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.
[7] Sunawapatse madzi anthu otopa, ndipo unawamana chakudya anthu anjala,
[8] ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake, munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.
[9] Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu, ndipo unapondereza ana amasiye.
[10] Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira, nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,
[11] nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu, nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.
[12] “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!
[13] Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani? Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?
[14] Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’
[15] Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale imene anthu oyipa ankayendamo?
[16] Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane, maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.
[17] Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni! Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’
[18] Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino, choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.
[19] “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera; anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.
[20] Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka ndipo moto wawononga chuma chawo!’
[21] “Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere; ukatero udzaona zabwino.
[22] Landira malangizo a pakamwa pake ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako.
[23] Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa; ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako,
[24] ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi, golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa.
[25] Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako, siliva wako wamtengowapatali.
[26] Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.
[27] Udzamupempha ndipo adzakumvera, ndipo udzapereka zimene unalonjeza.
[28] Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi, kuwala kudzakuwunikira pa njira yako.
[29] Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’ Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa.
[30] Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa, ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”