[1] Tsono Yobu anayankha kuti,
[2] “Achikhala mavuto anga anayezedwa, ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo!
[3] Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja; nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula.
[4] Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo; zoopsa za Mulungu zandizinga.
[5] Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu, nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya?
[6] Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere, nanga choyera cha dzira chimakoma?
[7] Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe; zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi.
[8] “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha, chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera,
[9] achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye, kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu!
[10] Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi, ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawu podziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo.
[11] “Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo? Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe?
[12] Kodi ine ndili ndi mphamvu? Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo?
[13] Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha, nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine?
[14] “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.
[15] Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga, ngati mitsinje imene imathamanga.
[16] Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula,
[17] koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe, ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo.
[18] Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi; iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu.
[19] Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi, anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo.
[20] Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi; koma akafika kumeneko, amangokhumudwako.
[21] Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza, mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha.
[22] Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake, ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu,
[23] ndilanditseni mʼdzanja la mdani, ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’
[24] “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete; ndionetseni pomwe ndalakwitsa.
[25] Ndithu, mawu owona ndi opweteka! Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani?
[26] Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena, ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe?
[27] Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye ndi kumugulitsa bwenzi lanu.
[28] “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana. Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu?
[29] Fewani mtima, musachite zosalungama; ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe.
[30] Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga? Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa?