Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:38

[1] Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,

[2] “Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe? Koma ndani angakhale chete wosayankhula?

[3] Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri, momwe walimbitsira anthu ofowoka.

[4] Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa; unachirikiza anthu wotha mphamvu.

[5] Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima, zakukhudza ndipo uli ndi mantha.

[6] Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako? Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako?

[7] “Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse? Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa?

[8] Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa, ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo.

[9] Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu; amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake.

[10] Mikango imabangula ndi kulira, komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa.

[11] Mkango umafa chifukwa chosowa nyama, ndipo ana amkango amamwazikana.

[12] “Mawu anabwera kwa ine mwamseri, makutu anga anamva kunongʼona kwake.

[13] Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku, nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato,

[14] ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera ndipo mafupa anga onse anaweyeseka.

[15] Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga, ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo.

[16] Chinthucho chinayimirira koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani. Chinthu chinayima patsogolo panga, kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti,

[17] ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu? Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake?

[18] Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe, ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa,

[19] nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi, amene maziko awo ndi fumbi, amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!

[20] Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa; mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya.

[21] Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu, kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’

Yobu — Chapters