Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:32

[1] “Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe? Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo?

[2] Mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru imawononga wopusa.

[3] Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa.

[4] Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe; amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza.

[5] Anthu anjala amamudyera zokolola zake, amamutengera ndi za pa minga pomwe, ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.

[6] Pakuti masautso satuluka mʼfumbi, ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi.

[7] Komatu munthu amabadwira kuti azunzike monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga.

[8] “Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu; ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye.

[9] Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.

[10] Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi, ndipo amathirira minda ya anthu.

[11] Iye amakweza anthu wamba, ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.

[12] Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu.

[13] Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo, ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.

[14] Mdima umawagwera nthawi yamasana; nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku.

[15] Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo; amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu.

[16] Choncho osauka ali ndi chiyembekezo, ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa.

[17] “Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.

[18] Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo; Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa.

[19] Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi, mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe.

[20] Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa, ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga.

[21] Adzakuteteza kwa anthu osinjirira, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika.

[22] Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi.

[23] Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako, ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere.

[24] Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa; udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo.

[25] Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri, ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi.

[26] Udzafika ku manda utakalamba, monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake.

[27] “Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona, choncho uzimvere ndi kuzitsata.”

Yobu — Chapters