Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:33

[1] Yehova anati kwa Yobu:

[2] “Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse? Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!”

[3] Pamenepo Yobu anayankha Yehova:

[4] “Ine sindili kanthu konse, kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga.

[5] Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho, ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.”

[6] Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti,

[7] “Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna; ndikufunsa mafunso ndipo iwe undiyankhe.

[8] “Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama? Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?

[9] Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu, ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu?

[10] Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola, ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu.

[11] Tsanula ukali wako wosefukirawo, uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse,

[12] Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse, uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.

[13] Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi; ukulunge nkhope zawo mʼmanda.

[14] Ukatero Ine ndidzakuvomereza kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi.

[15] “Taganiza za mvuwu, imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe, ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.

[16] Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga kwambiri!

[17] Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.

[18] Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa, nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.

[19] Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu, komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.

[20] Imapeza chakudya chake ku mtunda ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.

[21] Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta, imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.

[22] Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta; imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.

[23] Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha, iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.

[24] Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza kapena kuyikola mu msampha?

Yobu — Chapters