[1] Yesu analowa mʼbwato nawoloka, ndipo anabwera ku mudzi wa kwawo.
[2] Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo,“Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”
[3] Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.”
[4] Ndipo podziwa maganizo awo Yesu anati,“Bwanji mukuganiza zoyipa mʼmitima mwanu?
[5] Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’
[6] Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo,‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ ”
[7] Ndipo munthuyo anayimirira napita kwawo.
[8] Gulu la anthu litaona izi, linadzazidwa ndi mantha ndipo linalemekeza Mulungu amene anapereka ulamuliro kwa anthu.
[9] Ndipo Yesu atachoka kumeneko, anaona munthu wina dzina lake Mateyu, atakhala mʼnyumba ya msonkho. Anati kwa iye,“Nditsate Ine.” Ndipo iye ananyamuka namutsata.
[10] Ndipo pamene Iye ankadya mʼnyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anabwera nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake.
[11] Ndipo Afarisi poona izi, anati kwa ophunzira ake, “Nʼchifukwa chiyani Aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”
[12] Yesu atamva, anati,“Munthu wamoyo safuna singʼanga ayi, koma wodwala.
[13] Koma pitani kaphunzireni tanthauzo la mawu awa: ‘Ndimafuna chifundo osati nsembe ayi.’ Pakuti sindinabwere kudzayitana olungama koma ochimwa.”
[14] Ndipo ophunzira a Yohane anabwera namufunsa Iye kuti, “Bwanji ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”
[15] Yesu anayankha kuti,“Kodi oyitanidwa ku ukwati angamalire bwanji pamene mkwati ali naye pamodzi? Nthawi idzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa ndi pamene adzasala kudya.”
[16] Ndipo palibe munthu amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale chifukwa chigambacho chidzachoka ndipo chibowocho chidzakula kuposa kale.
[17] Kapena sathira vinyo watsopano mʼmatumba akale; akatero, matumba akalewo adzaphulika ndipo vinyoyo adzatayika, matumbawo adzawonongeka; satero ayi. Amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso ndipo zonse zimasungika.
[18] Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo.”
[19] Yesu ndi ophunzira ake ananyamuka napita naye pamodzi.
[20] Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake.
[21] Iyeyo anati mwa iye yekha, “Nditangokhudza kasonga ka mkanjo wake, ine ndidzachiritsidwa.”
[22] Ndipo Yesu anatembenuka namuona mayiyo nati,“Limbani mtima mayi iwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthawi yomweyo mayiyo anachiritsidwa.
[23] Yesu atalowa mʼnyumba ya mkulu wa sunagoge ndi kuona oyimba zitoliro ndi gulu la anthu ochita phokoso,
[24] anati,“Tulukani, mtsikanayu sanafe koma ali mtulo.” Koma anamuseka Iye.
[25] Atangowatulutsa anthuwo, analowa mʼnyumba ndipo anagwira dzanja la mtsikanayo ndipo anauka.
[26] Mbiriyi inamveka mʼdera lonse.
[27] Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!”
[28] Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti,“Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?” Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.”
[29] Pomwepo anakhudza maso awo nati,“Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.”
[30] Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati,“Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi.”
[31] Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse.
[32] Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula.
[33] Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, “Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli.”
[34] Koma Afarisi anati, “Akutulutsa mizimu yoyipa ndi mphamvu ya mkulu wa ziwanda.”
[35] Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo.
[36] Ataona maguluwo, anagwidwa ndi chisoni chifukwa anali ozunzika ndi osowa chithandizo ngati nkhosa zopanda mʼbusa.
[37] Pamenepo anati kwa ophunzira ake,“Zokolola ndi zambiri koma antchito ndi ochepa.
[38] Nʼchifukwa chake, pemphani Ambuye mwini zokolola kuti atumize antchito ku munda wake.”