[1] “Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe.
[2] Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo.
[3] “Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako?
[4] Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, ‘Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako?
[5] Wachiphamaso iwe! Yamba wachotsa chimtengo chili mʼdiso mwako ndipo pamenepo udzatha kuona bwino ndi kuchotsa kachitsotso kali mʼdiso mwa mʼbale wako.
[6] “Musapatse agalu zinthu zopatulika; kapena musaponyere nkhumba ngale zanu. Pakuti ngati mutero, zidzaziponda ndipo pomwepo zidzakutembenukirani ndi kukudulani nthulinthuli.
[7] “Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani.
[8] Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.
[9] “Ndani mwa inu, mwana wake akamupempha buledi amamupatsa mwala?
[10] Kapena ngati mwana apempha nsomba, kodi amamupatsa njoka?
[11] Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?
[12] Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.
[13] “Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo.
[14] Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.
[15] “Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa.
[16] Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula?
[17] Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa.
[18] Mtengo wabwino sungabale chipatso choyipa, ndi mtengo woyipa sungabale chipatso chabwino.
[19] Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.
[20] Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira.
[21] “Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.
[22] Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’
[23] Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’
[24] “Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe.
[25] Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe.
[26] Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga.
[27] Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”
[28] Yesu atamaliza kunena zonsezi, magulu a anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake,
[29] chifukwa anaphunzitsa ngati amene anali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo.