Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:21

[1] Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu.

[2] Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.”

[3] Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo.

[4] Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.”

[5] Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri.

[6] Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri.

[7] Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe.

[8] Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”

[9] Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe;

[10] ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende.

[11] Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake.

[12] Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.

[13] Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda.

[14] Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.

[15] Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”

[16] Yesu anawayankha kuti,“Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”

[17] Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”

[18] Koma Iye anati,“Bweretsani kwa Ine.”

[19] Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu.

[20] Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri.

[21] Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.

[22] Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo.

[23] Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha.

[24] Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.

[25] Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja.

[26] Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.

[27] Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti,“Limbani mtima! Ndine, musaope.”

[28] Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”

[29] Iye anati,“Bwera.” Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu.

[30] Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”

[31] Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati,“Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”

[32] Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka.

[33] Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”

[34] Atawoloka, anafika ku Genesareti.

[35] Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye.

[36] Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Mateyu — Chapters