Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:02

[1] Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti,

[2] “Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”

[3] Yesu anayankha kuti,“Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu?

[4] Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’

[5] Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’

[6] iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu.

[7] Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,

[8] “ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.

[9] Amandilambira Ine kwachabe ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”

[10] Yesu anayitana gulu la anthu nati,“Mverani ndipo zindikirani.

[11] Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”

[12] Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”

[13] Iye anayankha kuti,“Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe.

[14] Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”

[15] Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”

[16] Yesu anawafunsa kuti,“Kani ngakhale inunso simumvetsa?

[17] Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi?

[18] Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa.

[19] Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.

[20] Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”

[21] Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni.

[22] Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”

[23] Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”

[24] Iye anayankha kuti,“Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha.”

[25] Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!”

[26] Iye anayankha kuti,“Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.”

[27] Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”

[28] Pomwepo Yesu anayankha kuti,“Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.

[29] Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi.

[30] Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye ndi anthu olumala, osaona, ofa ziwalo, osayankhula ndi ena ambiri nawagoneka pa mapazi ake ndipo Iye anawachiritsa.

[31] Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.

[32] Yesu anayitana ophunzira ake nati,“Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira.”

[33] Ophunzira anayankha kuti, “Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?”

[34] Yesu anawafunsa kuti,“Muli ndi malofu a buledi angati?” Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono.”

[35] Iye anawuza gululo kuti likhale pansi.

[36] Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo.

[37] Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri.

[38] Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana.

[39] Yesu atatha kuwuza gululo kuti lipite kwawo, analowa mʼbwato ndipo anapita kudera la Magadala.

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Mateyu — Chapters