[1] Yesu anayankhula nawonso mʼmafanizo, nati,
[2] “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna.
[3] Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.
[4] “Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’
[5] “Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake.
[6] Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha.
[7] Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.
[8] “Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera.
[9] Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’
[10] Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.
[11] “Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati.
[12] Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete.
[13] “Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’
[14] “Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.”
[15] Kenaka Afarisi anatuluka nakakonza njira zomupezera zifukwa Yesu mʼmawu ake.
[16] Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani?
[17] Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”
[18] Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati,“Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa?
[19] Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari,
[20] ndipo anawafunsa kuti,“Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?”
[21] Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.” Pamenepo anawawuza kuti,“Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
[22] Atamva izi, anadabwa, ndipo anamusiya Iye, nachoka.
[23] Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso.
[24] Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
[25] Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo.
[26] Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri.
[27] Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso.
[28] Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”
[29] Yesu anayankha kuti,“Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu.
[30] Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba.
[31] Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,
[32] ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”
[33] Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.
[34] Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi.
[35] Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati,
[36] “Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?”
[37] Yesu anayankha kuti,“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.
[38] Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse.
[39] Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’
[40] Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”
[41] Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti,
[42] “Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”
[43] Iye anawawuza kuti,“Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,
[44] “Ambuye anati kwa Ambuye wanga: ‘Khala pa dzanja langa lamanja mpaka ndiyike adani ako pansi pa mapazi ako.’
[45] Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?”
[46] Panalibe wina anatha kuyankha, ndipo kuchokera pamenepo, panalibe wina anayerekeza kumufunsa funso.