Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:50

[1] Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu.

[2] Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”

[3] Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.

[4] Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[5] Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.

[6] Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi.

[7] Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[8] Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.

[9] Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani.

[10] Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[11] Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.

[12] Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli.

[13] Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[14] Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.

[15] Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi.

[16] Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[17] Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira.

[18] Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki.

[19] Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[20] Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira.

[21] Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela.

[22] Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[23] Zaka zonse za Enoki zinali 365.

[24] Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.

[25] Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki.

[26] Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[27] Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.

[28] Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna.

[29] Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”

[30] Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.

[31] Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.

[32] Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.

Genesis — Chapters