Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 8:29

[1] Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo.

[2] “Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo; mverani abambo anu Israeli.

[3] “Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa; mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga, wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.

[4] Wokokoma ngati madzi a chigumula, koma sudzakhalanso wopambana, iwe unagona pa bedi la abambo ako, ndithu unayipitsa bedi la mdzakazi wake.

[5] “Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo, anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano.

[6] Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri, kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo, pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.

[7] Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi ndi ukali wawo wankhanza choterewu! Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.

[8] “Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda; dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako; abale ako adzakugwadira iwe.

[9] Yuda ali ngati mwana wa mkango; umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga. Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi, ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?

[10] Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda, udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse, mpaka mwini wake weniweni atabwera ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.

[11] Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa, ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino. Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo; ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.

[12] Maso ake adzakhala akuda chifukwa cha vinyo, mano ake woyera chifukwa cha mkaka.

[13] “Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja; adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi; malire ake adzafika ku Sidoni.

[14] “Isakara ali ngati bulu wamphamvu wogona pansi pakati pa makola.

[15] Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira ndi kukongola kwa dziko lake, iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.

[16] “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.

[17] Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu, songo yokhala mʼnjira imene imaluma chidendene cha kavalo kuti wokwerapoyo agwe chagada.

[18] “Ndikuyembekeza chipulumutso chanu Yehova.

[19] “Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo, koma iye adzawathamangitsa.

[20] “Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma, ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu.

[21] “Nafutali ali ngati mbawala yayikazi yokhala ndi ana okongola kwambiri.

[22] “Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso, mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.

[23] Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza; anamuthamangitsa ndi mauta awo.

[24] Koma uta wake sunagwedezeke, ndi manja ake amphamvu aja analimbika, chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo, chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.

[25] Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza; chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa ndi mvula yochokera kumwamba, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.

[26] Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa madalitso a mapiri akale oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona. Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe, pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.

[27] “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa; umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha, ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”

[28] Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.

[29] Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti.

[30] Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda.

[31] Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya.

[32] Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”

[33] Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.

Genesis — Chapters