Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 13:16

[1] Patapita zaka ziwiri zathunthu, Farao analota atayimirira mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo,

[2] ndipo anangoona ngʼombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zooneka bwino ndi zonenepa zikutuluka mu mtsinje muja ndi kuyamba kudya msipu wa mu mawango.

[3] Kenaka ngʼombe zina zazikazi zisanu ndi ziwiri zosaoneka bwino ndi zowonda zinatulukanso mu mtsinje wa Nailo ndipo zinayimirira pambali pa zina zija zimene zinali mʼmphepete mwa mtsinje uja.

[4] Ndipo ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya ngʼombe zonenepa zija. Kenaka Farao anadzidzimuka.

[5] Posakhalitsa anagonanso ndipo analota kachiwiri: Analota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi labwino zitabala pa phata limodzi.

[6] Kenaka ngala zina zisanu ndi ziwiri zinaphuka. Izi zinali zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa.

[7] Ngala zowonda zija zinameza ngala zathanzi ndi zonenepa zija. Farao anadzidzimuka ndipo anaona kuti anali maloto chabe.

[8] Mmawa, Farao anavutika mu mtima kotero anayitanitsa amatsenga ndi anzeru onse a mu Igupto. Iwo atabwera, iye anawawuza maloto ake, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kutanthauzira malotowo kwa Farao.

[9] Ndipo mkulu wa operekera zakumwa anati kwa Farao, “Lero ndakumbukira kulephera kwanga.

[10] Paja nthawi ina Farao anapsera mtima antchito akefe, ndipo anatitsekera (ine ndi mkulu wa ophika buledi) mʼndende, mʼnyumba ya mkulu wa alonda.

[11] Tsiku lina tonse awiri tinalota maloto, ndipo loto lililonse linali ndi tanthauzo lake.

[12] Tsono momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, wantchito wa mkulu wa alonda. Ife tinamufotokozera maloto athu, ndipo anatitanthauzira malotowo. Munthu aliyense anamupatsa tanthauzo la loto lake.

[13] Ndipo zinthu zinachitikadi monga mmene anatitanthauzira. Ine anandibwezera pa ntchito yanga ndipo winayo anapachikidwa.”

[14] Choncho Farao anamuyitanitsa Yosefe, ndipo mofulumira anabwera naye kuchokera mʼdzenje muja. Ndipo atameta, ndi kusintha zovala, anapita kwa Farao.

[15] Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota maloto ndipo palibe amene watha kunditanthauzira. Tsono ndawuzidwa kuti iwe ukamva loto umadziwanso kulimasulira.”

[16] Yosefe anamuyankha Farao kuti, “Sindingathe koma Mulungu apereka yankho limene Farao akufuna.”

[17] Ndipo Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota nditayimirira mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo,

[18] ndipo ngʼombe zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zooneka bwino zinatuluka mu mtsinje muja ndi kumadya msipu wa mu mawango.

[19] Kenaka, ngʼombe zina zisanu ndi ziwiri zinatuluka. Izi zinali zosaoneka bwino ndiponso zowonda ndipo sindinaonepo ngʼombe zosaoneka bwino chonchi mʼdziko lonse la Igupto.

[20] Ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya zisanu ndi ziwiri zonenepa zimene zinatuluka poyamba zija.

[21] Koma ngakhale ngʼombezi zinadya zinazo, palibe amene akanatha kuzindikira kuti zinatero popeza zinali zosaonekabe bwino monga poyamba. Ndipo ndinadzidzimuka.

[22] “Nditagonanso kachiwiri, ndinalota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi ndi zonenepa zitabala pa phata limodzi.

[23] Kenaka panaphukanso ngala zina zisanu ndi ziwiri zofota, zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa.

[24] Ngala zowondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino zija. Ndinawawuza amatsenga koma palibe ndi mmodzi yemwe anatha kundimasulira.”

[25] Ndipo Yosefe anati kwa Farao, “Maloto awiriwa ndi ofanana ndipo ali ndi tanthauzo limodzi. Mulungu waululira Farao chimene atachite.

[26] Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Ndipo ngala zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Kutanthauza kwa maloto nʼkumodzi.

[27] Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndi zosaoneka bwino zimene zinatuluka pambuyozo ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zachabechabe, zowauka ndi mphepo ya kummawa zija ndi zaka zisanu ndi ziwiri za njala.

[28] “Tsono ndi monga ndafotokozeramu kuti Mulungu wakuwuziranitu zimene adzachite.

[29] Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zikubwera mu dziko lonse la Igupto,

[30] koma zidzatsatana ndi zaka zina zisanu ndi ziwiri za njala. Chakudya chochuluka cha mu Igupto chija chidzayiwalika ndipo njalayo idzawononga dziko.

[31] Zakudya zochuluka za mʼdzikomo zija sizidzakumbukirikanso chifukwa njala imene iti idzabwereyo idzakhala yoopsa.

[32] Popeza kuti malotowa aperekedwa kwa inu Mfumu kawiri, ndiye kuti Mulungu watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi posachedwapa.

[33] “Tsopano Farao apezeretu munthu wozindikira ndi wanzeru ndipo amuyike kukhala woyangʼanira dziko lonse la Igupto.

[34] Asankhenso akuluakulu a mʼdziko lino. Iwowa azitenga ndi kuyika padera limodzi la magawo asanu aliwonse a zokolola za mʼdziko muno mu zaka zonse zisanu ndi ziwiri za chakudya chochuluka.

[35] Iwo asonkhanitse zakudya zonse za mʼzaka zabwino zikubwerazi. Pansi pa ulamuliro wa Farao, akuluakuluwo asonkhanitse ndi kusunga bwino tirigu mʼmizinda yonse.

[36] Chakudya chimenechi chisungidwe kuti chidzagwiritsidwe ntchito mʼzaka zisanu ndi ziwiri za njala imene ikubwerayo mu Igupto, kuti anthu a mʼdzikoli asadzafe ndi njalayo.”

[37] Farao ndi nduna zake anagwirizana nawo malangizo a Yosefe.

[38] Choncho Farao anafunsa nduna zake nati, “Kodi tingathe kumupeza munthu wina ngati uyu, amene ali ndi mzimu wa Mulungu?”

[39] Farao anati kwa Yosefe, “Pakuti Mulungu wakudziwitsa iwe zonsezi, palibe wina wodziwa zinthu ndi wanzeru ngati iwe.

[40] Iwe ukhala nduna yayikulu mu dziko langa ndipo anthu onse adzamvera zimene walamula. Ine ndekha ndiye amene ndidzakuposa mphamvu chifukwa ndimakhala pa mpando waufumu.”

[41] Choncho Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndikukuyika iwe kukhala nduna yoyangʼanira dziko lonse la Igupto.”

[42] Ndipo Farao anavula mphete ku chala chake nayiveka ku chala cha Yosefe. Anamuvekanso mkanjo wonyezimira ndi nkufu wagolide mʼkhosi mwake.

[43] Anamukweza Yosefe pa galeta ngati wachiwiri pa ulamuliro. Ndipo anthu anafuwula pamaso pake nati, “Mʼgwadireni!” Motero anakhala nduna yayikulu ya dziko lonse la Igupto.

[44] Kenaka Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndine Farao; tsono iwe ukapanda kulamula, palibe amene akhoza kuchita chilichonse ngakhale kuyenda kumene mʼdziko lonse la Igupto.”

[45] Farao anamupatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-Panea ndipo anamupatsanso Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni, kuti akhale mkazi wake. Choncho Yosefe anayendera dziko lonse la Igupto.

[46] Yosefe anali ndi zaka 30 pamene amayamba ntchito kwa Farao, mfumu ya ku Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pa maso pa Farao nayendera dziko lonse la Igupto.

[47] Mʼzaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zambiri zija, anthu mʼdzikomo anakolola zochuluka.

[48] Yosefe anasonkhanitsa zakudya zonse zokololedwa mʼzaka zisanu ndi ziwiri zija ndipo anazisunga mʼmizinda. Mu mzinda uliwonse anayikamo chakudya chimene chinalimidwa mʼminda yozungulira komweko.

[49] Yosefe anasunga tirigu wochuluka kwambiri ngati mchenga wa ku nyanja. Kunali tirigu wochuluka kwambiri motero kuti analeka nʼkulembera komwe.

[50] Zisanafike zaka zanjala, Yosefe anabereka ana aamuna awiri mwa Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni.

[51] Yosefe anamutcha mwana wake woyamba, Manase popeza anati, “Mulungu wandiyiwalitsa zovuta zanga zija ndiponso banja la abambo anga.”

[52] Mwana wachiwiri wa mwamuna anamutcha Efereimu popeza anati, “Mulungu wandipatsa ana mʼdziko la masautso anga.”

[53] Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zija zinatha,

[54] ndipo zaka zisanu ndi ziwiri za njala zija zinayamba monga ananenera Yosefe. Njalayi inafika ku mayiko ena onse koma ku dziko lonse la Igupto kunali chakudya.

[55] Pamene njala ija inakwanira dziko lonse la Igupto anthu analilira Farao kuti awapatse chakudya. Koma Farao anawawuza kuti, “Pitani kwa Yosefe ndipo mukachite zimene akakuwuzeni.”

[56] Pamene njala inafalikira dziko lonse, Yosefe anatsekula nkhokwe za zakudya namagulitsa tirigu kwa anthu a ku Igupto aja, pakuti njala inafika poyipa kwambiri mu Igupto monse.

[57] Anthu ankabwera ku Igupto kuchokera ku mayiko ena onse kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inafika poyipa kwambiri pa dziko lonse lapansi.

Genesis — Chapters