Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 8:38

[1] Israeli anasonkhanitsa zonse anali nazo napita ku Beeriseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa abambo ake Isake.

[2] Ndipo Mulungu anayankhula ndi Israeli mʼmasomphenya usiku nati, “Yakobo! Yakobo!” Iye anayankha, “Ee, Ambuye.”

[3] Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu.

[4] Ine ndidzapita ku Igupto pamodzi ndi iwe ndipo mosakayika konse zidzukulu zako ndidzazibweretsa konkuno. Yosefe adzakhalapo pa nthawi yako yomwalira.”

[5] Yakobo anachoka ku Beeriseba, ndipo ana ake anakweza abambo awo, ana awo, pamodzi ndi akazi awo pa ngolo zimene Farao anatumiza kuti adzakwerepo.

[6] Iwo anatenganso ziweto zawo ndi katundu wawo amene anali naye ku Kanaani, ndipo Yakobo pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake anapita ku Igupto.

[7] Ndiye kuti popita ku Igupto Yakobo anatenga ana aamuna, zidzukulu zazimuna, ana aakazi ndi zidzukulu zazikazi.

[8] Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto: Rubeni mwana woyamba wa Yakobo.

[9] Ana aamuna a Rubeni ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi.

[10] Ana aamuna a Simeoni ndi awa: Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo amene mayi wake anali wa ku Kanaani.

[11] Ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.

[12] Ana aamuna a Yuda ndi awa: Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani. Ana a Perezi anali li3 Hezironi ndi Hamuli.

[13] Ana aamuna a Isakara ndi awa: Tola, Puwa, Yobi ndi Simironi.

[14] Ana aamuna a Zebuloni ndi awa: Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.

[15] Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33.

[16] Ana aamuna a Gadi ndi awa: Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.

[17] Ana aamuna a Aseri ndi awa: Imuna, Isiva, Isivi, Beriya ndi Sera mlongo wawo. Ana aamuna a Beriya ndi awa: Heberi ndi Malikieli.

[18] Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16.

[19] Ana aamuna a Rakele mkazi wa Yakobo anali: Yosefe ndi Benjamini.

[20] Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu.

[21] Ana aamuna a Benjamini ndi awa: Bela, Bekeri, Asibeli, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi.

[22] Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa mkazi wake Rakele. Onse analipo khumi ndi anayi.

[23] Mwana wa mwamuna wa Dani anali: Husimu.

[24] Ana aamuna a Nafutali ndi awa: Yahazeeli, Guni, Yezeri ndi Silemu.

[25] Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Biliha amene Labani anapereka kwa mwana wake Rakele. Onse pamodzi analipo asanu ndi awiri.

[26] Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66.

[27] Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.

[28] Tsopano Yakobo anatumiza Yuda kwa Yosefe kukamupempha kuti akakumane naye ku Goseni. Iwo atafika ku chigawo cha Goseni,

[29] Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali.

[30] Israeli anati kwa Yosefe, “Tsopano ndikhoza kumwalira poti ndaona nkhope yako kuti ukanali ndi moyo.”

[31] Ndipo Yosefe anati kwa abale ake pamodzi ndi a pa banja la abambo ake, “Ndipita kwa Farao ndipo ndikamuwuza kuti, ‘Abale anga pamodzi ndi onse a mʼnyumba ya abambo anga amene amakhala mʼdziko la Kanaani abwera kuno kwa ine.

[32] Anthuwa ndi abusa; amaweta ziweto zawo ndipo abwera ndi nkhosa ndi ngʼombe zawo, pamodzi ndi antchito awo.’

[33] Tsono Farao akakuyitanani nakufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’

[34] Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.”

Genesis — Chapters