Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:10

[1] Choncho Isake anayitanitsa Yakobo namudalitsa nʼkumuwuzitsa kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanaani.

[2] Panopo upite ku Padanaramu, ku nyumba kwa Betueli abambo a amayi akowa, kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa amayi akowa.

[3] Mulungu Wamphamvuzonse akudalitse iwe nakupatse ana ambiri mpaka udzasanduke gulu lalikulu la mitundu ya anthu.

[4] Mulunguyo akudalitse iwe monga mmene anamudalitsira Abrahamu kuti zidzukulu zako zidzalandira dziko limene ukukhalamo ngati mlendo kuti lidzakhale lawo. Ili ndi dziko limene Mulungu anapereka kwa Abrahamu.”

[5] Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau.

[6] Tsopano Esau anadziwa kuti Isake anadalitsa Yakobo ndi kumutumiza ku Padanaramu kuti akakwatire kumeneko. Anawuzidwanso kuti, “Usakwatire mkazi wa ku Kanaani.”

[7] Yakobo anamvera abambo ake ndi amayi ake ndi kupita ku Padanaramu.

[8] Ndiye pamenepo Esau anazindikira kuti abambo ake Isake sankakondwera ndi akazi a ku Kanaani;

[9] anapita kwa Ismaeli mwana wa Abrahamu nakwatira Mahalati mwana wa Ismaeli, mlongo wake wa Nebayoti. Anatero kuwonjezera akazi amene anali nawo kale.

[10] Yakobo ananyamuka pa ulendo kuchoka ku Beeriseba kupita ku Harani.

[11] Atafika pa malo pena, anayima kuti agonepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Anatenga mwala wina pomwepo natsamiritsapo mutu wake, ndipo anagona.

[12] Mʼmaloto, anaona makwerero oyimikidwa pansi ndipo anakafika kumwamba. Angelo a Mulungu amakwera ndi kutsika pa makwereropo.

[13] Tsono Yehova anayimirira pambali pake, nati, “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu kholo lake la Isake abambo ako. Ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako dziko limene ukugonamolo.

[14] Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako.

[15] Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.”

[16] Yakobo atadzidzimuka, anati, “Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe.”

[17] Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.”

[18] Mmamawa mwake Yakobo anatenga mwala umene anatsamira mutu wake uja nawuyimika ngati chipilala ndi kuthira mafuta pamwamba pake

[19] Iye anawatcha malowo Beteli, ngakhale kuti poyamba mzindawo ankawutcha Luzi.

[20] Pamenepo Yakobo analumbira kwa Yehova nati, “Ngati inu Mulungu mukhala ndi ine, kundiyangʼanira pa ulendo wangawu ndi kundipatsa chakudya ndi chovala;

[21] ngati inu mudzandibweretsa kwathu mu mtendere, ndiye kuti mudzakhala Mulungu wanga,

[22] ndipo mwala uwu ndawuyimikawu udzakhala Nyumba ya Mulungu. Ine ndidzakupatsani chakhumi cha zinthu zonse zimene mudzandipatse.”

Genesis — Chapters