Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:41

[1] Yehova anawuza Mose kuti,

[2] “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:

[3] “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere.

[4] Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni,

[5] kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.

[6] “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.

[7] “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori

[8] ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi,

[9] ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.

[10] “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu.

[11] Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti.

[12] Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere. “ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”

[13] Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka,

[14] chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo.

[15] Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”

[16] Yehova anawuza Mose kuti,

[17] “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni.

[18] Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo.

[19] Mayina awo ndi awa: Kalebe mwana wa Yefune, wochokera ku fuko la Yuda,

[20] Semueli mwana wa Amihudi, wochokera ku fuko la Simeoni;

[21] Elidadi mwana wa Kisiloni, wochokera ku fuko la Benjamini;

[22] Buki mwana wa Yogili, mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;

[23] Hanieli mwana wa Efodi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;

[24] Kemueli mwana wa Sifitani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.

[25] Elizafani mwana wa Parinaki, mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;

[26] Palitieli mwana wa Azani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,

[27] Ahihudi mwana wa Selomi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;

[28] Pedaheli mwana wa Amihudi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”

[29] Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.

Numeri — Chapters