Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 11:50

[1] Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni,

[2] “Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.”

[3] Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti,

[4] “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:

[5] Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi: kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki; kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu;

[6] kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi.

[7] Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.

[8] Mwana wa Palu anali Eliabu,

[9] ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova.

[10] Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo.

[11] Koma ana a Kora sanafe nawo.

[12] Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;

[13] kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera; kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli.

[14] Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.

[15] Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi: kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni; kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi; kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni;

[16] kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini; kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri;

[17] kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi; kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli.

[18] Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.

[19] Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.

[20] Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Sela, fuko la Asera; kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi; kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera.

[21] Zidzukulu za Perezi zinali izi: kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli.

[22] Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.

[23] Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Tola, fuko la Atola; kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa;

[24] kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu. Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi.

[25] Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.

[26] Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi; kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni; kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli.

[27] Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500.

[28] Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:

[29] Zidzukulu za Manase: kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi); kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi.

[30] Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi; kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri; kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki;

[31] kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli; kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu;

[32] kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida; kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi.

[33] (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)

[34] Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.

[35] Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi; kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela; kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri; kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani.

[36] Zidzukulu za Sutela zinali izi: kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani.

[37] Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo.

[38] Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Bela, fuko la Abela; kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli; kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu;

[39] kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu; kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu;

[40] Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi: kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi; kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani;

[41] Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.

[42] Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu. Izi zinali zidzukulu za Dani.

[43] Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.

[44] Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna; kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi; kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya;

[45] ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya: kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi; kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli;

[46] (Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera)

[47] Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.

[48] Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli; kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni;

[49] kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri; kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu.

[50] Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.

[51] Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.

[52] Yehova anawuza Mose kuti,

[53] “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo.

[54] Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa.

[55] Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo.

[56] Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”

[57] Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa: kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni; kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati; kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari.

[58] Awanso anali mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, fuko la Kora banja la Akohati, li4 (Kohati anali abambo a Amramu.

[59] Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo.

[60] Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.

[61] Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).

[62] Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.

[63] Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko.

[64] Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai;

[65] Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Numeri — Chapters