Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 9:33

[1] Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,

[2] “Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi.

[3] Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali.

[4] Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi.

[5] Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa: Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,

[6] Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni,

[7] Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,

[8] Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara,

[9] Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni,

[10] Mwa ana a Yosefe: kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi; kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri;

[11] Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini,

[12] Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani,

[13] Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri,

[14] Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi,

[15] Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.”

[16] Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli.

[17] Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa,

[18] ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi

[19] monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:

[20] Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[21] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.

[22] Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[23] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300.

[24] Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[25] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.

[26] Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[27] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.

[28] Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[29] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.

[30] Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[31] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400. li4

[32] Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[33] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.

[34] Kuchokera mwa zidzukulu za Manase: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[35] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200.

[36] Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[37] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.

[38] Kuchokera mwa zidzukulu za Dani: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[39] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.

[40] Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[41] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.

[42] Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali: Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.

[43] Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.

[44] Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake.

[45] Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo.

[46] Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550.

[47] Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena.

[48] Pakuti Yehova anawuza Mose kuti,

[49] “Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli.

[50] Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.

[51] Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa.

[52] Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake.

[53] Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”

[54] Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.

Numeri — Chapters