Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:48

[1] Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe.

[2] Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.

[3] Ngati wina adziyesa kanthu pamene iyeyo sali kanthu konse, akudzinamiza yekha.

[4] Munthu aliyense aziyesa yekha ntchito zake mmene zilili. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, iyeyo asadzifanizire ndi munthu wina wake,

[5] pakuti aliyense ayenera kusenza katundu wake.

[6] Koma munthu amene akuphunzira mawu, agawireko mphunzitsi wake zinthu zonse zabwino zimene iye ali nazo.

[7] Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa.

[8] Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

[9] Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.

[10] Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.

[11] Onani zilembo zazikulu zimene ine ndikulemba ndi dzanja langa.

[12] Onse amene akufuna kuoneka abwino pamaso pa anthu akukukakamizani kuti muchite mdulidwe. Akuchita izi ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti apewe kuzunzidwa chifukwa cha mtanda wa Khristu.

[13] Pakuti ngakhale iwowa amene anachita mdulidwe satsata Malamulo, komabe akufuna kuti muchite mdulidwe kuti anyadire mdulidwe wanuwo.

[14] Ine sindingathe kunyadira kanthu kena koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu, kudzera mwa mtandawo dziko lapansi linapachikidwa kwa ine ndi ine ku dziko lapansi.

[15] Pakuti kaya mdulidwe kapena kusachita mdulidwe, sizitanthauza kanthu; chofunika ndi kulengedwa mwatsopano.

[16] Mtendere ndi chifundo zikhale kwa onse amene amatsata chiphunzitso ichi, ndi pa Israeli wa Mulungu.

[17] Pomaliza wina asandivutitse, pakuti mʼthupi mwanga muli zizindikiro za Yesu.

[18] Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu zikhale ndi mzimu wanu abale. Ameni.

Kalata ya Paulo Yolembera Agalatiya — Chapters