Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:20

[1] Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu. Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu:

[2] Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.

[3] Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.

[4] Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake,

[5] Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake.

[6] Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda.

[7] Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu

[8] chimene anatipatsa mosawumira. Mwa nzeru zonse ndi chidziwitso,

[9] Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake.

[10] Chimene anakonza kuti chichitike nʼchakuti, ikakwana nthawi yake asonkhanitsa pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za kumwamba ndi pa dziko lapansi.

[11] Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake,

[12] nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake.

[13] Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.

[14] Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.

[15] Choncho, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse,

[16] ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga.

[17] Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni.

[18] Ndimapempheranso kuti maso a mitima yanu atsekuke ndi cholinga choti mudziwe chiyembekezo chimene Iye anakuyitanirani, chuma cha ulemerero chomwe chili mwa anthu oyera mtima.

[19] Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu zake zazikulu koposa zimene zili mwa ife amene timakhulupirira. Mphamvuyi ndi yofanana ndi mphamvu yoposa ija

[20] imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba.

[21] Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo.

[22] Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo,

[23] umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse.

Kalata ya Paulo Yolembera Aefeso — Chapters