Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:08

[1] Paulo mtumwi, osati wosankhidwa ndi anthu kapena kutumidwa ndi munthu ayi, koma Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate amene anamuukitsa Yesuyo kwa akufa,

[2] pamodzi ndi abale onse amene ali nane, Kulembera mipingo ya ku Galatiya:

[3] Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.

[4] Yesuyo anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu kuti atipulumutse ku njira za moyo woyipa uno, molingana ndi chifuniro cha Mulungu ndi Atate athu.

[5] Ulemerero ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ameni.

[6] Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana,

[7] umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu.

[8] Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa!

[9] Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”

[10] Kodi tsopano ndikufuna kukopa anthu kuti andivomereze, kapena Mulungu? Kapena ndikufuna kukondweretsa anthu? Ngati ine ndikanakhala kuti ndikufunabe kukondweretsa anthu, sindikanakhala mtumiki wa Khristu.

[11] Abale, ine ndikufuna kuti mudziwe, kuti Uthenga Wabwino umene ndinalalikira si ochokera kwa munthu ayi.

[12] Ine sindinawulandire kuchokera kwa munthu aliyense, kapena kuphunzitsidwa; koma ndinawulandira mwa vumbulutso lochokera kwa Khristu.

[13] Pakuti inu munamva za moyo wanga wakale mʼChiyuda, mmene ndinkazunzira mpingo wa Mulungu koopsa ndi kuyesetsa kuwuwononga.

[14] Ine ndinkapambana Ayuda ambiri a msinkhu wanga pochita za Chiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa pa miyambo ya makolo athu.

[15] Koma Mulungu, amene anandipatula ine ndisanabadwe, ndi kundiyitana mwachisomo chake, atakondweretsedwa

[16] kuvumbulutsa Mwana wake mwa ine, kuti ndikalalikire Khristuyo pakati pa anthu a mitundu ina, ine sindinapemphe nzeru kwa munthu aliyense.

[17] Ine sindinapite ku Yerusalemu kukaonana ndi amene anali atumwi ine ndisanakhale mtumwi. Mʼmalo mwake nthawi yomweyo ndinapita ku Arabiya ndi kubwereranso ku Damasiko.

[18] Pambuyo pake, patatha zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu kukaonana ndi Petro ndikukhala naye masiku khumi ndi asanu.

[19] Ine sindinaonane ndi atumwi enawo koma Yakobo yekha, mʼbale wa Ambuye.

[20] Ine ndikutsimikizira inu pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberani si zonama ayi.

[21] Pambuyo pake ndinapita ku Siriya ndi ku Kilikiya.

[22] Koma sindimadziwika ndi nkhope ku mipingo ya ku Yudeya imene ili mwa Khristu.

[23] Iwo anangomva mbiri yokha yakuti, “Munthu amene poyamba anatizunza ife, tsopano akulalikira chikhulupiriro chimene iyeyo nthawi ina anafuna kuchiwononga.”

[24] Ndipo iwo anayamika Mulungu chifukwa cha ine.

Kalata ya Paulo Yolembera Agalatiya — Chapters