Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:44

[1] Iye anati, “Inu abale anga ndi makolo anga, tamvani mawu akudziteteza kwanga.”

[2] Atamva iye akuyankhula Chihebri, anakhala chete. Kenaka Paulo anati,

[3] “Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero.

[4] Ine ndinkazunza anthu otsatira Njirayi mpaka kuwapha. Ndinkagwira amuna ndi amayi ndi kuwayika mʼndende.

[5] Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe.

[6] “Nthawi ya masana, nditayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunandizungulira.

[7] Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti,‘Saulo! Saulo! Ukundizunziranji?’ ”

[8] Ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?” Iye anayankha kuti,“Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.”

[9] Anzanga a paulendo anaona kuwalako, koma sanamve mawuwo, a Iye amene amayankhula nane.

[10] Ine ndinafunsa kuti,“Kodi ndichite chiyani Ambuye?” Ambuye anati,“Imirira ndipo pita ku Damasiko. Kumeneko adzakuwuza zonse zimene ukuyenera kuchita.”

[11] Anzanga anandigwira dzanja kupita nane ku Damasiko, popeza kuwala kunja kunandichititsa khungu.

[12] “Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu.

[13] Iye anayimirira pafupi nane nati, ‘Mʼbale Saulo, penyanso!’ Ndipo nthawi yomweyo ndinapenya ndikumuona iyeyo.

[14] “Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake.

[15] Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva.

[16] Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.’

[17] “Nditabwerera ku Yerusalemu, ndikupemphera mʼNyumba ya Mulungu, ndinachita ngati ndakomoka.

[18] Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti,‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’ ”

[19] Ine ndinayankha Ambuye kuti, “Anthu awa akudziwa kuti ine ndinkapita ku sunagoge iliyonse ndipo ndinkawaponya mʼndende ndi kuwakwapula amene ankakhulupirira inu.

[20] Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”

[21] Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti,“Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.”

[22] Gulu la anthu linamvetsera mawu a Paulo mpaka pamene ananena izi, kenaka anakweza mawu awo nafuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi! Ngosayenera kukhala moyo!”

[23] Akufuwula ndi kuponya zovala zawo ndi kuwaza fumbi kumwamba,

[24] mkulu wa asilikali analamulira kuti amutenge Paulo kupita naye ku malo a asilikali. Iye analamula kuti Paulo akwapulidwe kwambiri ndi kumufunsa kuti apeze chimene anthu ankafuwulira chotere.

[25] Atamumanga kuti amukwapule, Paulo anati kwa msilikali wolamulira asilikali 100 amene anayima pamenepo, “Kodi malamulo amalola kukwapula nzika ya Chiroma imene sinapezedwe yolakwa?”

[26] Wolamulira asilikali 100 uja atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali ndi kumufotokozera. Iye anafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani ndi munthuyu amene ndi nzika ya Chiroma?”

[27] Mkulu wa asilikali uja anapita kwa Paulo ndipo anamufunsa kuti, “Tandiwuze, kodi ndiwe nzika ya Chiroma?” Paulo anayankha kuti, “Inde.”

[28] Kenaka mkulu wa asilikaliyo anati, “Ine ndinapereka ndalama zambiri kuti ndikhale nzika.” Paulo anayankha kuti, “Koma ine ndinabadwa nzika.”

[29] Iwo amene anati amufunse analeka nthawi yomweyo. Mkulu wa asilikali uja anachita mantha atazindikira kuti wamanga Paulo amene ndi nzika ya Chiroma.

[30] Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.

Machitidwe a Atumwi — Chapters