Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:23

[1] Mʼbuku langa loyamba, ndinakulembera iwe Teofilo zonse zimene Yesu anayamba kuchita ndi kuphunzitsa,

[2] mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba, mwamphamvu ya Mzimu Woyera, atawalangiza atumwi amene anawasankha.

[3] Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi.

[4] Nthawi ina atasonkhana nawo pamodzi, Yesu analamulira ophunzira ake kuti,“Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate anga analonjeza yomwe ndinakuwuzani.

[5] Pakuti Yohane anakubatizani ndi madzi, koma posachedwapa inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”

[6] Atumwi atasonkhana pamodzi, iwo anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi nthawi ino mubwezeretsa ufumu kwa Israeli?”

[7] Yesu anawawuza kuti,“Sikofunika kuti mudziwe za nthawi kapena masiku amene Atate ayika mwa ulamuliro wawo.

[8] Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

[9] Atatha kuyankhula zimenezi, Yesu anatengedwa kupita kumwamba ophunzira ake akuona, ndipo anabisika mʼmitambo.

[10] Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo.

[11] Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”

[12] Pamenepo atumwi anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri la Olivi, mtunda wosakwana kilomita kuchokera mu mzindamo.

[13] Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo.

[14] Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

[15] Pa nthawi imeneyo Petro anayimirira pakati pa okhulupirira (gulu la anthu pafupifupi 120).

[16] Iye anati, “Abale anga, Malemba anayenera kukwaniritsidwa omwe Mzimu Woyera anayankhula kalekale kudzera mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolera amene anamugwira Yesu.

[17] Iye anali mmodzi wa gulu lathu ndipo anatumikira pamodzi ndi ife.”

[18] (Yudasi anagula munda ndi ndalama zimene anazipeza pochita zoyipa zija; kumeneko, iye anagwa chamutu, naphulika pakati ndipo matumbo ake wonse anakhuthuka.

[19] Aliyense mu Yerusalemu anamva zimenezi, kotero anatcha mundawo mʼchiyankhulo chawo kuti Akeledama, kutanthauza, Munda wa Magazi).

[20] Petro anati, “Pakuti kwalembedwa mʼbuku la Masalimo kuti, “Nyumba yake isanduke bwinja, ndipo pasakhale wogonamo. Ndiponso, “Wina atenge ntchito yake yautsogoleri.

[21] Chifukwa chake ndi kofunika kusankha mmodzi wa anthu amene akhala nafe nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankayenda nafe,

[22] kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.”

[23] Pamenepo anasankha anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba (wodziwikanso kuti Yusto) ndi Matiyasi.

[24] Kenaka iwo anapemphera nati, “Ambuye mukudziwa mtima wa aliyense. Tionetseni amene mwamusankha mwa awiri awa

[25] kuti atenge ntchito iyi ya utumwi, imene Yudasi anasiya napita kumalo womuyenera.”

[26] Tsono anachita maere, ndipo maerewo anagwera Matiyasi. Tsono iye anawonjezedwa pa gulu la atumwi khumi ndi mmodziwo.

Machitidwe a Atumwi — Chapters