Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:47

[1] Atumwi ndi abale a ku Yudeya konse anamva kuti anthu a mitundu ina analandiranso Mawu a Mulungu.

[2] Tsono Petro atafika ku Yerusalemu, abale amene anali a mdulidwe anamutsutsa iye,

[3] ndipo anati, “Iwe unalowa mʼnyumba ya anthu osachita mdulidwe ndi kudya nawo.”

[4] Koma Petro anayamba kuwafotokozera zonse mwatsatanetsatane momwe zinachitikira kuti,

[5] “Ine ndimapemphera mu mzinda wa Yopa ndipo ndili ngati wokomoka ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chokhala ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba chogwiridwa msonga zake zinayi, ndipo chinatsikira pa ine.

[6] Ine ndinayangʼana mʼkati mwake ndipo ndinaona nyama za miyendo inayi za mʼdziko lapansi, zirombo, zokwawa, ndi mbalame zamlengalenga.

[7] Kenaka ine ndinamva mawu akuti,‘Petro, Imirira. Ipha, nudye.’

[8] “Ine ndinayankha kuti, ‘Ayi, Ambuye! Pakuti chinthu chodetsedwa ndi chonyansa sindinadyepo pakamwa pangapa.’

[9] “Mawu ochokera kumwamba ananenanso kachiwiri kuti,‘Chimene Mulungu wachiyeretsa usanene kuti ndi chodetsedwa.’

[10] Zimenezi zinachitika katatu ndipo kenaka zonse zinatengedwa kupita kumwamba.

[11] “Nthawi yomweyo anthu atatu amene anatumidwa kuchokera ku Kaisareya anayima pa nyumba yomwe ndimakhalayo.

[12] Mzimu anandiwuza kuti ndisakayike, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi awa anapitanso nane ndipo tinalowa mʼnyumba ya munthuyo.

[13] Iye anatiwuza mmene anaonera mngelo atayimirira mʼnyumba mwake ndi kumuwuza kuti, ‘Tumiza anthu ku Yopa kuti akayitane Simoni wotchedwa Petro.

[14] Iye adzakuwuza uthenga umene udzapulumutsa iwe ndi a pa banja ako.’

[15] “Nditangoyamba kuyankhula, Mzimu Woyera anafika pa iwo monga momwe anafikira pa ife poyamba paja.

[16] Kenaka ndinakumbukira zimene Ambuye ananena kuti,‘Yohane anabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’

[17] Tsono ngati Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyo imene anatipatsa ife, amene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti nditsutsane ndi Mulungu?”

[18] Iwo atamva zimenezi analibenso chonena ndipo anayamika Mulungu nati, “Potero Mulungu wapatsa anthu a mitundu ina mwayi wotembenuka mtima ndi kulandira moyo.”

[19] Tsopano amene anabalalika chifukwa cha mazunzo amene anayamba ataphedwa Stefano, anapita mpaka ku Foinike, ku Kupro ndi ku Antiokeya, ndipo ankalalikira kwa Ayuda okha.

[20] Komabe, ena pakati pawo ochokera ku Kupro ndi ku Kurene anapita ku Antiokeya ndipo iwo anayamba kuyankhulanso kwa Agriki, nawawuza za Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.

[21] Mphamvu ya Ambuye inali nawo ndipo anthu ambiri anakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.

[22] Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya.

[23] Atafika ndi kuona chisomo cha Mulungu pa iwo, anakondwa ndi kuwalimbikitsa anthu onsewo kuti apitirire kukhala woona mu mtima mwa Ambuye.

[24] Barnabayo anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro ndipo gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Ambuye.

[25] Kenaka Barnaba anapita ku Tarisisi kukafuna Saulo,

[26] ndipo pamene anamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Barnaba ndi Saulo anasonkhana ndi mpingo kwa chaka chimodzi naphunzitsa anthu ambirimbiri. Okhulupirirawo anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.

[27] Masiku amenewo ku Antiokeya kunafika aneneri ena ochokera ku Yerusalemu.

[28] Mmodzi wa iwo dzina lake Agabu, anayimirira ndipo Mzimu anamutsogolera kunenera zamʼtsogolo kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lapansi. (Izi zinachitikadi nthawi ya ulamuliro wa Klaudiyo).

[29] Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya.

[30] Izi anazichitadi ndipo anatuma Barnaba ndi Saulo kukapereka mphatsozo kwa akulu a mpingo.

Machitidwe a Atumwi — Chapters