[1] Ana a Israeli anali awa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni,
[2] Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri.
[3] Ana a Yuda anali awa: Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha.
[4] Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.
[5] Ana a Perezi anali awa: Hezironi ndi Hamuli.
[6] Ana a Zera anali awa: Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu.
[7] Mwana wa Karimi anali Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.
[8] Mwana wa Etani anali Azariya.
[9] Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali: Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai.
[10] Ramu anabereka Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda.
[11] Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi,
[12] Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese.
[13] Yese anabereka Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea,
[14] wachinayi Netaneli, wachisanu Radai,
[15] wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide.
[16] Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli.
[17] Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli.
[18] Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni.
[19] Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri.
[20] Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli.
[21] Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu.
[22] Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi.
[23] (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.
[24] Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa.
[25] Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali: Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya.
[26] Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu.
[27] Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa: Maazi, Yamini ndi Ekeri.
[28] Ana a Onamu anali awa: Shamai ndi Yada. Ana a Shamai anali awa: Nadabu ndi Abisuri.
[29] Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi.
[30] Ana a Nadabu anali awa: Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana.
[31] Ana a Apaimu anali awa: Isi, amene anabereka Sesani. Sesani anabereka Ahilai.
[32] Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa: Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana.
[33] Ana a Yonatani anali awa: Peleti ndi Zaza. Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli.
[34] Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha. Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha.
[35] Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi.
[36] Atayi anali abambo ake a Natani, Natani anali abambo ake a Zabadi,
[37] Zabadi anali abambo a Efilali, Efilali anali abambo a Obedi,
[38] Obedi anali abambo a Yehu, Yehu anali abambo a Azariya,
[39] Azariya anali abambo a Helezi, Helezi anali abambo a Eleasa,
[40] Eleasa anali abambo ake a Sisimai, Sisimai anali abambo a Salumu,
[41] Salumu anali abambo a Yekamiya, Yekamiya anali abambo a Elisama.
[42] Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa: Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni.
[43] Ana a Hebroni anali awa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema.
[44] Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai.
[45] Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri.
[46] Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi.
[47] Ana a Yahidai anali awa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi.
[48] Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana.
[49] Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa.
[50] Izi zinali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa: Sobala abambo a Kiriati Yearimu,
[51] Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera.
[52] Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi: Harowe, theka la banja la Manahati,
[53] ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa.
[54] Zidzukulu za Salima zinali izi: Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori,
[55] ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.