[1] Adamu, Seti, Enosi
[2] Kenani, Mahalaleli, Yaredi,
[3] Enoki, Metusela, Lameki, Nowa.
[4] Ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti.
[5] Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
[6] Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima
[7] Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
[8] Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani
[9] Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
[10] Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.
[11] Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
[12] Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori.
[13] Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti,
[14] Ayebusi, Aamori, Agirigasi
[15] Ahivi, Aariki, Asini
[16] Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
[17] Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
[18] Aripakisadi anabereka Sela ndipo Selayo anabereka Eberi:
[19] Eberi anabereka ana aamuna awiri: wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
[20] Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
[21] Hadoramu, Uzali, Dikila
[22] Obali, Abimaeli, Seba,
[23] Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
[24] Semu, Aripakisadi, Sela
[25] Eberi, Pelegi, Reu
[26] Serugi, Nahori, Tera
[27] ndi Abramu (amene ndi Abrahamu).
[28] Ana a Abrahamu ndi awa: Isake ndi Ismaeli.
[29] Zidzukulu zake zinali izi: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu,
[30] Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema,
[31] Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli.
[32] Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa: Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. Ana a Yokisani ndi awa: Seba ndi Dedani
[33] Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura.
[34] Abrahamu anabereka Isake. Ana a Isake anali awa: Esau ndi Israeli.
[35] Ana aamuna a Esau anali awa: Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora.
[36] Ana a Elifazi anali awa: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi: Amene anabereka ndi Timna: Amaleki.
[37] Ana a Reueli anali awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza.
[38] Ana a Seiri anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.
[39] Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
[40] Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana.
[41] Mwana wa Ana anali Disoni. Ana a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani
[42] Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Yaakani. Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani.
[43] Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko: Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
[44] Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
[45] Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake.
[46] Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
[47] Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake.
[48] Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake.
[49] Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
[50] Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
[51] Hadadi anamwaliranso. Mafumu a ku Edomu anali: Timna, Aliva, Yeteti,
[52] Oholibama, Ela, Pinoni,
[53] Kenazi, Temani, Mibezari,
[54] Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu.