Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:38

[1] Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu.

[2] Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova.

[3] Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.

[4] Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli.

[5] Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga,

[6] ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.

[7] Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:

[8] Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.

[9] Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando; nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.

[10] Nyadirani dzina lake loyera; ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova.

[11] Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi zonse.

[12] Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita, zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake,

[13] inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.

[14] Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi.

[15] Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse, mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda,

[16] pangano limene anachita ndi Abrahamu, lonjezo limene analumbira kwa Isake.

[17] Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo, kwa Israeli monga pangano lamuyaya.

[18] “Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani monga cholowa chimene udzachilandira.”

[19] Ali anthu owerengeka, ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo,

[20] iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina, ku ufumu wina kupita ku ufumu wina.

[21] Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze; chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu:

[22] “Musakhudze odzozedwa anga; musawachitire choyipa aneneri anga.”

[23] Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi; lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

[24] Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse, ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.

[25] Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda; Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.

[26] Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake, koma Yehova analenga kumwamba.

[27] Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake; mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye.

[28] Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,

[29] perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake. Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake; pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake.

[30] Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi! Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe.

[31] Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere; anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!”

[32] Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo; minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo!

[33] Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba, idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova, pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

[34] Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala mpaka muyaya.

[35] Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu, mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina, kuti tiyamike dzina lanu loyera, kuti tikutamandeni.”

[36] Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.”

[37] Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse.

[38] Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata.

[39] Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni

[40] kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli.

[41] Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.”

[42] Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.

[43] Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.

1 Mbiri — Chapters