[1] Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo.
[2] Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata.
[3] Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo,“Imirira, bwera kuno kutsogolo.”
[4] Ndipo Yesu anawafunsa kuti,“Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.
[5] Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo,“Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira.
[6] Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu.
[7] Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata.
[8] Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni.
[9] Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize.
[10] Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze.
[11] Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!”
[12] Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.
[13] Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye.
[14] Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira
[15] ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda.
[16] Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro);
[17] Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu);
[18] Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote,
[19] ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
[20] Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye.
[21] Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”
[22] Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”
[23] Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati:“Kodi Satana angatulutse bwanji Satana?
[24] Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse.
[25] Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima.
[26] Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha.
[27] Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera.
[28] Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa,
[29] koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”
[30] Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”
[31] Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye.
[32] Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”
[33] Iye anafunsa kuti,“Amayi ndi abale anga ndi ndani?”
[34] Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati,“Awa ndi amayi anga ndi abale anga!
[35] Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”