[1] Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu,
[2] monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya: “Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu, amene adzakonza njira yanu,”
[3] “Mawu a wofuwula mʼchipululu, ‘Konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.’ ”
[4] Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo.
[5] Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani.
[6] Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo.
[7] Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake.
[8] Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
[9] Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani.
[10] Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda.
[11] Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
[12] Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu,
[13] ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
[14] Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati,
[15] “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
[16] Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi.
[17] Yesu anati,“Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”
[18] Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
[19] Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo.
[20] Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.
[21] Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa.
[22] Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo.
[23] Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti,
[24] “Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
[25] Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati,“Khala chete! Tuluka mwa iye!”
[26] Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.
[27] Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.”
[28] Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira.
[29] Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya.
[30] Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye.
[31] Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.
[32] Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda.
[33] Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo,
[34] Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.
[35] Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera.
[36] Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye,
[37] ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”
[38] Yesu anayakha kuti,“Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.”
[39] Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.
[40] Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
[41] Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati,“Ndikufuna, yeretsedwa!”
[42] Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.
[43] Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti,
[44] “Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.”
[45] Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.