[1] Yesu atazindikira kuti Afarisi amva zoti Iye ankapeza ndi kubatiza ophunzira ambiri kupambana Yohane,
[2] (ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake).
[3] Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya.
[4] Ndipo Iye anayenera kudutsa mu Samariya.
[5] Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.
[6] Chitsime cha Yakobo chinali pamenepo ndipo Yesu atatopa ndi ulendo anakhala pansi pambali pa chitsimecho. Nthawi inali pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi masana.
[7] Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye,“Kodi ungandipatse madzi akumwa.”
[8] (Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya).
[9] Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).
[10] Yesu anamuyankha kuti,“Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”
[11] Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti?
[12] Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?”
[13] Yesu anayankha kuti,“Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu,
[14] koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”
[15] Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.”
[16] Iye anamuwuza kuti,“Pita kayitane mwamuna wako ndipo ubwere naye.”
[17] Iye anayankha kuti, “Ine ndilibe mwamuna.” Yesu anati kwa iye,“Wakhoza ponena kuti ulibe mwamuna.
[18] Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.”
[19] Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri.
[20] Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”
[21] Yesu anati,“Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu.
[22] Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda.
[23] Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna.
[24] Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”
[25] Mayiyo anati, “Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife.”
[26] Ndipo Yesu anamuwuza kuti,“Amene ndikukuyankhulane, ndine amene.”
[27] Pa nthawi yomweyo ophunzira ake anabwerera ndipo anadabwa kupeza Iye akuyankhula ndi mayi. Koma palibe amene anamufunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” kapena, “Nʼchifukwa chiyani mukuyankhula naye?”
[28] Kenaka mayiyo anasiya mtsuko wamadzi, nabwerera ku mzinda ndipo anati kwa anthu,
[29] “Tiyeni mukaone munthu amene wandiwuza ine zilizonse zimene ndinazichita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu?”
[30] Iwo anatuluka mʼmudziwo ndi kupita kumene kunali Iye.
[31] Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, “Rabi idyani.”
[32] Koma Iye anawawuza kuti,“Ine ndili ndi chakudya choti ndidye chimene inu simukuchidziwa.”
[33] Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?”
[34] Yesu anati,“Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake.
[35] Kodi inu simunena kuti, ‘Kwatsala miyezi inayi ndipo kenaka kukolola?’ Ine ndikukuwuzani kuti, tsekulani maso anu ndipo muyangʼane mʼminda! Mbewu zacha kale kuti zikololedwe.
[36] Ngakhale tsopano amene akukolola akulandira malipiro ake, ndipo akututa mbewu ku moyo wosatha kuti wofesa ndi wokolola asangalale pamodzi.
[37] Nʼchifukwa chake mawu akuti, ‘Wina amafesa ndipo wina amakolola’ ndi woona.
[38] Ine ndinakutumani kukakolola zimene simunagwirire ntchito. Ena anagwira ntchito yolemetsa ndipo inu mwatuta phindu la ntchito yawo.”
[39] Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.”
[40] Choncho Asamariya atabwera kwa Iye, anamuwumiriza Iye kuti akhale nawo, ndipo Iye anakhala nawo masiku awiri.
[41] Ndipo chifukwa cha mawu ake, ena ambiri anakhulupirira.
[42] Iwo anati kwa mayiyo, “Ife sitikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha, koma tsopano ife tadzimvera tokha, ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndithu ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi.”
[43] Patatha masiku awiri Iye anachoka napita ku Galileya.
[44] (Tsopano Yesu mwini ananena kale kuti mneneri salandira ulemu mʼdziko lake).
[45] Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.
[46] Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo.
[47] Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.
[48] Yesu anawawuza iwo kuti,“Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira.”
[49] Nduna ya mfumuyo inati, “Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe.”
[50] Yesu anayankha kuti,“Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka.
[51] Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira.
[52] Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, “Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri.”
[53] Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye,“Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira.
[54] Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.