Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:04

[1] Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko,

[2] ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo.

[3] Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”

[4] Yesu anayankha kuti,“Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”

[5] Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”

[6] Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.

[7] Yesu anati kwa antchitowo,“Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.

[8] Ndipo Iye anatinso kwa iwo,“Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.” Iwo anachita momwemo.

[9] Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali

[10] ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”

[11] Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.

[12] Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka.

[13] Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu.

[14] Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo.

[15] Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo.

[16] Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati,“Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!”

[17] Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”

[18] Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?”

[19] Yesu anawayankha kuti,“Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”

[20] Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?”

[21] Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake.

[22] Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.

[23] Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake.

[24] Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse.

[25] Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Yohane — Chapters