[1] Tsoka kwa mzinda wa anthu opondereza, owukira ndi odetsedwa!
[2] Sumvera aliyense, sulandira chidzudzulo. Sumadalira Yehova, suyandikira pafupi ndi Mulungu wake.
[3] Akuluakulu ake ali ngati mikango yobuma, olamulira ake ndi olusa ngati mimbulu ya nthawi ya madzulo, zimene pofika mmawa sizisiya chilichonse.
[4] Aneneri ake ndi odzikuza; anthu achinyengo. Ansembe ake amadetsa malo opatulika ndipo amaphwanya lamulo.
[5] Yehova amene ali pakati pawo ndi wolungama; Iye salakwa. Tsiku ndi tsiku amaweruza molungama, ndipo tsiku lililonse salephera, komabe ochita zoyipa sachita manyazi nʼkomwe.
[6] “Ndachotseratu mitundu ya anthu; ndagwetsa malinga awo. Ndipo sindinasiye ndi mmodzi yemwe mʼmisewu mwawo, popanda aliyense wodutsa. Mizinda yawo yawonongedwa; palibe aliyense adzatsalemo.
[7] Ndinati, ‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa ndi kumvera kudzudzula kwanga!’ Ndipo sindidzawononga nyumba zawo, kapena kuwalanganso. Koma iwo anali okonzeka kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita.
[8] Choncho mundidikire,” akutero Yehova, “chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni. Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu, kusonkhanitsa maufumu ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo; mkwiyo wanga wonse woopsa. Dziko lonse lidzatenthedwa ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga.
[9] “Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova ndi kumutumikira Iye pamodzi.
[10] Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi anthu anga ondipembedza, omwazikana, adzandibweretsera zopereka.
[11] Tsiku limenelo simudzachita manyazi chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira, popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo. Simudzakhalanso odzikuza mʼphiri langa lopatulika.
[12] Koma ndidzasiya pakati panu anthu ofatsa ndi odzichepetsa, amene amadalira dzina la Yehova.
[13] Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika; sadzayankhulanso zonama, ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo. Adzadya ndi kugona ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”
[14] Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni; fuwula mokweza, iwe Israeli! Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!
[15] Yehova wachotsa chilango chako, wabweza mdani wako. Yehova, Mfumu ya Israeli, ali pakati pako; sudzaopanso chilichonse.
[16] Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti, “Usaope, iwe Ziyoni; usafowoke.
[17] Yehova Mulungu wako ali pakati pako, ali ndi mphamvu yopulumutsa. Adzakondwera kwambiri mwa iwe, adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake, adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”
[18] “Ndidzakuchotserani zowawa za pa zikondwerero zoyikika; nʼzolemetsa ndi zochititsa manyazi.
[19] Taonani, nthawi imeneyo ndidzathana ndi onse amene anakuponderezani; ndidzapulumutsa olumala ndi kusonkhanitsa amene anamwazika. Ndidzawayamikira ndi kuwachitira ulemu mʼdziko lililonse mmene anachititsidwa manyazi.
[20] Pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani; pa nthawi imeneyo ndidzakubweretsani ku mudzi kwanu. Ndidzakuyamikirani ndi kukuchitirani ulemu pakati pa mitundu ya anthu a dziko lapansi pamene ndidzabwezeretsa mtendere wanu inu mukuona,” q4 akutero Yehova.