[1] Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.
[2] Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso.
[3] Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu.
[4] Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.
[5] Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
[6] Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’ ” (ndiko, kukatsitsa Khristu)
[7] “kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa).
[8] Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira,
[9] kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
[10] Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.
[11] Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”
[12] Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye
[13] pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”
[14] Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo?
[15] Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”
[16] Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?”
[17] Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.
[18] Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”
[19] Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti, “Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake. Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”
[20] Ndipo Yesaya molimba mtima akuti, “Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna. Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”
[21] Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti, “Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga kwa anthu osandimvera ndi okanika.”