[1] Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu. Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu.
[2] Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu.
[3] Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
[4] Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga.
[5] Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse.
[6] Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu.
[7] Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye.
[8] Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita,
[9] komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu,
[10] ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga Onesimo, amene ndamubala ndili mu unyolo.
[11] Anali wopanda phindu kwa iwe, koma tsopano wasanduka wa phindu kwa iwe ndi kwa inenso.
[12] Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni.
[13] Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino.
[14] Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza.
[15] Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse.
[16] Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye.
[17] Tsono ngati umati ndine mnzako, umulandire iyeyu monga momwe ukanandilandirira ineyo.
[18] Ngati anakulakwira kapena kukongola kanthu kalikonse, ndidzalipira ineyo.
[19] Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo.
[20] Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu.
[21] Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi.
[22] Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.
[23] Epafra, wamʼndende mnzanga chifukwa cha Khristu Yesu akupereka moni.
[24] Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni.
[25] Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.